Leviticus 21

Malamulo a Ansembe

1Yehova anawuza Mose kuti, “Yankhula ndi ansembe, ana a Aaroni, ndipo uwawuze kuti, ‘Wansembe asadzidetse pokhudza munthu wakufa pakati pa abale ake. 2Koma akhoza kukhudza thupi lakufa la amayi ake, abambo ake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi, mchimwene wake, 3kapena mlongo wake wosakwatiwa amene amadalira iye chifukwa sanakwatiwe. Iye akhoza kudzidetsa pokhudza thupi lakufa la mchemwali wake wosakwatiwa yekha. 4Koma wansembe asadzidetse chifukwa cha anthu amene ali nawo pa ubale obwera chifukwa cha ukwati.

5“ ‘Ansembe asamete tsitsi kumutu kwawo kapena mʼmphepete mwa ndevu zawo, kapenanso kudzichekacheka pa thupi lawo. 6Ayenera kukhala oyera pamaso pa Mulungu wawo ndipo asachititse manyazi dzina la Mulungu wawo. Popeza amapereka nsembe zotentha pa moto kwa Yehova, chakudya cha Mulungu wawo, iwo azikhala woyera.

7“ ‘Asakwatire akazi amene adzidetsa ndi chiwerewere kapena akazi amene amuna awo awasudzula, chifukwa ansembe ndi oyera pamaso pa Mulungu wawo. 8Iwo akhale oyera chifukwa amapereka nsembe kwa Mulungu wanu. Muziwaona kuti ndi oyera, popeza Ine Yehova amene ndimawayeretsa ndine woyera, nawonso akhale oyera.

9“ ‘Ngati mwana wamkazi wa wansembe adziyipitsa pochita zachiwerewere, ndiye kuti iye akuchititsa manyazi abambo ake; mwanayo atenthedwe pa moto.

10“ ‘Munthu amene ali mkulu wa ansembe pakati pa abale ake, amene anamudzoza pomutsanulira mafuta pamutu pake, ndiponso amene anapatulidwa pomuveka zovala zaunsembe, asalekerere tsitsi lake kapena kungʼamba zovala zake kusonyeza kuti ali pa chisoni. 11Asalowe mʼnyumba mmene muli munthu wakufa ngakhale womwalirayo ndi amayi ake kapena abambo ake. 12Asadzidetse potulukira kunja kwa malo opatulika popeza mafuta womupatula kukhala wansembe ali pamutu pake. Ine ndine Yehova.

13“ ‘Iye akwatire namwali wosadziwa mwamuna. 14Asakwatire mkazi wamasiye, mkazi wosudzulidwa, kapena mkazi wachiwerewere, koma akwatire namwali wosadziwa mwamuna pakati pa anthu a mtundu wake, 15kuti mtundu wake usakhale wodetsedwa pakati pa abale popeza ndine Yehova, amene ndimamuyeretsa.’ ”

16Yehova anawuza Mose kuti, 17“Muwuze Aaroni kuti, ‘Munthu aliyense mwa zidzukulu zake ku mibado yawo yonse ikubwera akakhala ndi chilema asabwere kudzapereka nsembe kwa Mulungu wake. 18Munthu aliyense wachilema motere: munthu wakhungu kapena wolumala miyendo, munthu wolumala nkhope kapena waziwalo zambiri, 19munthu wa phazi lolumala kapena dzanja lolumala, 20kapena munthu wokhota msana kapena wamfupi kwambiri, kapena wolumala maso, munthu wa nthenda yonyerenyetsa, kapena wamphere, kapenanso wophwanyika mavalo, sayenera kusendera pafupi. 21Mdzukulu aliyense wa Aaroni wansembe, amene ali ndi chilema asadzayandikire kukapereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Popeza kuti ali ndi chilema, asayandikire kudzapereka nsembe ya chakudya kwa Mulungu wake. 22Koma iye angathe kudya chakudya chopatulika kwambiri chija, ngakhalenso chakudya chotsala pa nsembe zopatulika. 23Koma chifukwa cha kulumala kwake, sayenera kuyandikira katani kapena kufika pa guwa kuti angadetse malo anga wopatulika. Ine ndine Yehova, amene ndimawayeretsa.’ ”

24Choncho Mose anawuza Aaroni ndi ana ake pamodzi ndi Aisraeli onse zimenezi.

Copyright information for NyaCCL